Malawi
This article was added by the user . TheWorldNews is not responsible for the content of the platform.

PHOTOS: ‘Akakamirana Pogonana Ngati Agalu M’boma La Dowa’

Anthu wochuluka akhamukira ku polisi ya Mponela m’boma la Dowa komwe akufuna kuona anthu omwe akuti mwina akanilirana akuchita zadama.

Malinga ndi anthu omwe tinawafunsa koma anakana kuti tiwajambule ati nawo anangomva anthu ena akunena kuti nkutheka akanilirana pamalo ena ogona alendo pa Mponela.

Mneneri wa apolisi ku Mponela, a Macferson Msadala, ati naonso akudabwa ndi momwe anthu afikila pa ofesi yao chifukwa nkhaniyi sanailandire.

 “Anthuwa tinawatenga kuti afike adzionere okha m’ma ofesi athu ndipo apeza kuti anthuwa sitinawabise kuno, koma anthu ambili akufikabe kuno ku ofesi yathu zomwe zikutidabwitsa,” atelo a Msadala.

Komabe a Msadala ati nkutheka kuti anthu ena angofuna kufalitsa nkhani zabodza zomwe ati zimasokoneza bata kudera ndipo iwo ngati apolisi akudzudzula mchitidwewu.

Malipoti osatsimikizika ati pa Mponela m’boma la Dowa pali malo ogona kapena kucheza alendo oposa mazana awili (200).-(Wolemba Mayeso Chikhadzula, MBC Online).