Malawi
This article was added by the user . TheWorldNews is not responsible for the content of the platform.

Phungu wa Blantyre Malabada akhazikitsa thumba la ndalama pofuna kuthana ndi umphawi

Phungu waku Blantyre Malabada Constituency Hon. Ismail Rizzq Mkumba akhazikitsa Ndirande Trust Limited Lamulungu lino pa Nyambadwe Ground mumzinda wa Blantyre.

Malingana ndi a Mkumba zonse zokhudza mwambo-wu zafika kumapeto tsopano.

Iwo ati cholinga chawo chokhazikitsa Trust-yi ndikuthana ndi umphawi omwe wakuta m’dera lawo komanso kuno ku Malawi.

A Mkumba ati kudzera mu Trust-yi, akhazikitsa kampani zingapo zomwe zizipanga bizinesi.

Iwo ati phindu lomwe lizipezeka ku kampanizi aziligwilitsa ntchito popangira zitukuko zosiyanasiyana.

Kampani yoyamba kutsegulidwa ikhala yopanga madzi ya Ndirande Hill Water.

Phungu-yu wati anthu ayamba kugula umwini wakampanizi akakhazitsa Trust-yi lamulungu lino.

Aka ndikoyamba phungu kuno kuno ku Malawi kutsegula Trust ndi cholinga choti anthu m’dera lake azipindula